5 Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapitikitsa kuyambira pacipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.
6 Ndipo Yoswa anang'amba zobvala zace, nagwa nkhope yace pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akulu akulu a Israyeli, nathira pfumbi pamitu pao.
7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!
8 Ndidzanenanji, Ambuye, Israyeli atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?
9 Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?
10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako cotere?
11 Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.