7 Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordano, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordano!
8 Ndidzanenanji, Ambuye, Israyeli atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao?
9 Akadzamva ici Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzacitiranji dzina lanu lalikuru?
10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako cotere?
11 Israyeli wacimwa, nalakwiranso cipangano canga, ndinawalamuliraco; natengakonso coperekedwaco; anabanso, nanyenganso, naciika pakati pa akatundu ao.
12 Mwa ici ana a Israyeli sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga coperekedwaco, kucicotsa pakati pa inu.
13 Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Pali coperekedwa cionongeke pakati pako, Israyeli iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutacotsa coperekedwaco pakati panu.