16 Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapitikitse, nampitikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi.
17 Ndipo sanatsala mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Beteli osaturukira kwa Israyeli; nasiya mudzi wapululu, napitikitsa Israyeli.
18 Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungo iri m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lace kuloza mudzi.
19 Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lace, nalowa m'mudzi, naugwira; nafulumira nayatsa mudziwo.
20 Pamene amuna a ku Ai anaceuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa cakuno kapena cauko; ndi anthu othawira kucipululu anatembenukira owapitikitsa.
21 Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israyeli yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai.
22 A kumudzinso anawaturukira; potero anakhala pakati pa Israyeli, ena mbali yina, ena mbali yina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsala kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense.