2 ndipo anali ndi pakati; ndipo apfuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.
3 Ndipo cinaoneka cizindikilo cina m'mwamba, taonani, cinjoka cofiira, cacikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zacifumu zisanu ndi ziwiri.
4 Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.
5 Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wacifumu wace.
6 Ndipo mkazi anathawira kucipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.
7 Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi cinjoka; cinjokanso ndi angelo ace cinacita nkhondo;
8 ndipo sicinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba.