26 ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ici?
27 Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.
28 Ndipo m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.
29 Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa iye.
30 (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye)
31 Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga, naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
32 Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye, anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.