19 Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.
20 Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azicita yekha: ndipo adzamuonetsa nchito zoposa izi, kuti mukazizwe,
21 Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwanaapatsa moyo iwo amene iye afuna.
22 Pakuti Atate saweruza munthu ali yense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;
23 kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.
24 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.
25 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.