1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Seba mbiri ya Solomo yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa.
2 Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wace waukulu, ndi ngamila zakunyamula zonunkhira, ndi golidi wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomo anakamba naye zonse za m'mtima mwace.
3 Ndipo Solomo anamyankha miyambi yace yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozera iye.
4 Ndipo pamene mfumu yaikazi ya ku Seba adaona nzeru zonse za Solomo, ndi nyumba adaimangayo,
5 ndi zakudya za pa gome lace, ndi makhalidwe a anyamata ace, ndi maimiriridwe a atumiki ace, ndi zobvala zao, ndi otenga zikho ace, ndi nsembe yace yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.
6 Ndipo anati kwa mfumu, idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya macitidwe anu ndi nzeru zanu.