15 Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunacokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ace amene Yehova ananenetsa Abiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.
16 Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu Aisrayeli inu; yang'aniranitu, nyumba yako, Davide. Momwemo Aisrayeli anacoka kumka ku mahema ao.
17 Kama ana aja a Israyeli akukhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.
18 Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.
19 Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.
20 Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.
21 Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.