27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.
28 Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.
29 Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani.
30 Koma cinthu ici cinasanduka: chimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani.
31 Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu acabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.
32 Ndipo Yerobiamu anaika madyerero mwezi wacisanu ndi citatu, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m'Beteli, nawaphera nsembe ana a ng'ombe aja anawapanga, naika m'Beteli ansembe a misanje imene anaimanga.
33 Ndipo anapereka nsembe pa guwa la nsembe analimanga m'Beteli, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi citatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israyeli madyerero, napereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.