1 Ndipo caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda.
2 Anakhala mfumu zaka zitatu m'Yerusalemu, ndipo dzina la amace linali Maaka mwana wa Abisalomu.
3 Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wace, zimene iye adacita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wace sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wace monga mtima wa Davide kholo lace.
4 Koma cifukwa ca Davideyo Yehova Mulungu wace anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wace pambuyo pace, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;
5 cifukwa kuti Davide adacita colungama pamaso pa Yehova, osapambuka masiku ace onse pa zinthu zonse adamlamulira iye, koma cokhaco cija ca Uriya Mhiti.
6 Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu masiku onse a moyo wace.
7 Ndipo macitidwe ace ena a Abiya, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobiamu.