4 Koma iye mwini analowa m'cipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, cotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindiri wokoma woposa makolo anga.
5 Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.
6 Ndipo anaceuka, naona kumutu kunali kamkate kooca pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi,
7 Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kaciwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka.
8 Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvuya cakudya cimeneco masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika ku phiri la Mulungu ku Horebu.
9 Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Ucitanji pano, Eliya?
10 Ndipo anati, Ine ndinacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli anasiya cipangano canu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.