2 Natumiza mithenga lrumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati kwa iye,
3 Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golidi wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.
4 Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndiri nazo.
5 Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golidi wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;
6 koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti cifuniro conse ca maso ako adzacigwira ndi manja ao, nadzacicotsa.
7 Pamenepo mfumu ya Israyeli anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti-munthu uyu akhumba coipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golidi wanga; ndipo sindinamkaniza.
8 Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musabvomereze.