1 Mafumu 20:28-34 BL92

28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israyeli, nati, Atero: Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ici ndidzapereka unyinji uwu waukuru m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

29 Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israyeli anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.

30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'cipinda ca m'katimo.

31 Pamenepo anyamata ace anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israyeli ndi mafumu acifundo; tiyeni tibvale ciguduli m'cuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titurukire kwa mfumu ya Israyeli, kapena adzakusungirani moyo.

32 Motero anabvala ciguduli m'cuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israyeli, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.

33 Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni, Pamenepo Benihadadi anaturuka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'gareta mwaceo

34 Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samaria. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.