16 Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wamphesa wa Naboti, kuulandira.
17 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya waku Tisibe, nati,
18 Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israyeli, akhala m'Samariya; taona, ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.
19 Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, mulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agaru ananyambita mwazi wa Naboti, pompaja agaru adzanyambita mwazi wako, inde wako.
20 Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kucita coipaco pamaso pa Yehova.
21 Taona, ndidzakufikitsira coipa, ndi kucotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka m'lsrayeli;
22 ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi ya Basa mwana wa Ahiya; cifukwa ca kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kucimwitsa Israyeli.