9 Tsono mfumu ya Israyeli anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.
10 Ndipo mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zao zacifumu pabwalo pa khomo la cipata ca Samaria; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.
11 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti,
12 Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Gileadi, ndipo mudzacita mwai; popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.
13 Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri abvomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa m'modzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.
14 Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.
15 Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Gileadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzacita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.