3 Ndipo Solomo anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wace; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.
4 Ndipo mfumu inapita ku Gibeoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukuru unali kumeneko, Solomo anapereka nsembe zopsereza cikwi cimodzi pa guwalo la nsembe.
5 Ku Gibeoni Yehova anaonekera Solomo m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha cimene ndikupatse.
6 Ndipo Solomo anati, Munamcitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi coonadi ndi cilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira cokoma ici cacikuru kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wace wacifumu monga lero lino.
7 Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kuturuka kapena kulowa.
8 Ndipo kapolo wanu ndiri pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao.
9 Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?