6 Ndipo Solomo anati, Munamcitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi coonadi ndi cilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira cokoma ici cacikuru kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wace wacifumu monga lero lino.
7 Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kuturuka kapena kulowa.
8 Ndipo kapolo wanu ndiri pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao.
9 Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?
10 Ndipo mau amenewa anakondweretsa Yehova kuti Solomo anapempha cimeneci.
11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha cimeneci, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso cuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera mirandu;
12 taona, ndacita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.