1 Ndipo Hiramu mfumu ya ku Turo anatuma anyamata ace kwa Solomo, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wace; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.
2 Ndipo Solomo anatumiza mau kwa Hiramu, nati,
3 Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wace nyumba, cifukwa ca nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ace.
4 Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena coipa condigwera.
5 Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wacifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.
6 Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebano, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni.