1 Ndipo kunacitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, caka cacinai cakukhala Solomo mfumu ya Israyeli, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi waciwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.
2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.
3 Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.
4 Ndipo m'nvumbamo anamanga mazenera a made okhazikika.