2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.
3 Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.
4 Ndipo m'nvumbamo anamanga mazenera a made okhazikika.
5 Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kacisi, ndi monenera momwemo; namanga zipinda zozinga,
6 Cipinda capansico kupingasa kwace kunali mikono isanu, capakatico kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi, cacitatuco kupingasa kwace mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anacepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m'makoma a nyumba.
7 Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka: kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena cipangizo cacitsulo, pomangidwa iyo.
8 Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kutikira ku zipinda za pakati, ndi kuturuka m'zapakatizo kulowa m'zacitatuzo,