38 Ndipo anapanga mbiya zamphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikuru makumi anai, ndipo mbiya iri yonse inali ya mikono inai: pa phaka liri lonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
39 Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa kupenya kumwera.
40 Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga nchito yonse anaicitira mfumu Solomo ya m'nyumba ya Yehova.
41 Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo,
42 ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,
43 ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi ziri pa maphakawo,
44 ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale;