6 Ndipo anamanga khumbi la nsanamira, m'litali mwace munali mikono makumi asanu, kupingasa kwace mikono makumi atatu; ndipo panali khumbi lina patsogolo pace, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pacepo.
7 Ndipo anamanga khumbi la mpando wacifumu loweruziramo iye, ndilo khumbi la mirandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.
8 Ndipo nyumba yace yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khumbilo, linamangidwa cimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomo, yofanafana ndi khumbi limeneli.
9 Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, ya muyeso muyeso, yoceka ndi mipeni ya mano mana m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumazikokufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikuru,
10 Ndipo maziko ace anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu.
11 Ndi pamwamba pace panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wace, ndi mitengo yamkungudza.
12 Ndipo bwalo lalikuru lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungundza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi likole la nyumbayo.