13 Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naicha dzina lao, Dziko lacikole, kufikira lero lino.
14 Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri.
15 Ndipo cifukwa cace ca msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomo ndi cimeneci; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido; ndi Gezeri.
16 Pakuti Farao mfumu ya Aigupto adakwera nalanda Gezeri, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wace mkazi wa Solomo.
17 Ndipo Solomo anamanganso Gezeri, ndi Betihoroni wakunsi,
18 ndi Balati, ndi Tadimori wa m'cipululu m'dziko muja,
19 ndi midzi yonse yosungamo zinthu zace za Solomo, ndi midzi yosungamo magareta ace, ndi midzi yokhalamo apakavalo ace, ndi zina ziti zonse zidakomera Solomo kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.