23 Ameneyo anali akulu a akapitao oyang'anira nchito ya Solomo, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira nchito aja.
24 Koma mwana wamkazi wa Farao anaturuka m'mudzi wa Davide kukwera ku nyumba yace adammangira Solomo, pamenepo iye anamanganso Milo.
25 Ndipo caka cimodzi Solomo anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, pa guwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira pa guwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.
26 Ndipo mfumu Solomo anamanga zombo zambiri ku Ezioni Geberi uli pafupi ndi Eloti, pambali pa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.
27 Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ace m'zombozo amarinyero ozerewera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomo.
28 Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golidi matalenti mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomo.