14 pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, cikakhala coona, catsimikizika cinthuci, kuti conyansa cotere cacitika pakati pa inu;
15 muzikanthatu okhala m'mudzi muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuuononga konse, ndi zonse ziri m'mwemo, ng'ombe zace zomwe, ndi lupanga lakuthwa.
16 Ndipo muzikundika zofunkha zace zonse pakati pakhwalala pace, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zace zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.
17 Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka cinthu coti cionongeke; kuti Yehova a aleke mkwiyo wacewaukali, nakucitireni cifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukucurukitsani monga analumbirira makolo anu;
18 pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace onse amene ndikuuzani lero lino, kucita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.