2 Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakucita ciri coipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira cipangano cace,
3 nakatumikira milungu yina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;
4 ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsitsa, ndipo taonani, cikakhala coonadi, coti nzenizeni, conyansaci cacitika m'Israyeli;
5 pamenepo muturutse mwamunayo kapena mkaziyo, anacita coipaco, kumka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.
6 Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.
7 Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse, Potero muzicotsa coipaco pakati panu.
8 Ukakulakani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo mirandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kumka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;