13 Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.
14 Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kucita cotero.
15 Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;
16 monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebe, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso mota waukuru uwu, kuti tingafe.
17 Ndipo Yehova anati kwa ine, Cokoma ananenaci.
18 Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwace, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.
19 Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.