2 Alibe colowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wace ndiye colowa cao, monga ananena nao.
3 Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chipfu.
4 Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.
5 Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mapfuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza.
6 Ndipo Mlevi akacokera ku mudzi wanu wina m'Israyeli monse, kumene akhalako, nakadza ndi cifuniro conse ca moyo wace ku malo amene Yehova adzasankha;
7 pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wace, monga amacita abale ace onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.
8 Cakudya cao cizifanana, osawerengapo zolowa zace zogulitsa.