5 Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mapfuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza.
6 Ndipo Mlevi akacokera ku mudzi wanu wina m'Israyeli monse, kumene akhalako, nakadza ndi cifuniro conse ca moyo wace ku malo amene Yehova adzasankha;
7 pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wace, monga amacita abale ace onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.
8 Cakudya cao cizifanana, osawerengapo zolowa zace zogulitsa.
9 Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kucita mongamwa zonyansa za amitundu aja.
10 Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku mota wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.
11 Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.