30 Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu.
31 Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awacite m'dziko limene ndiwapatsa likhale lao lao.
32 Potero muzisamalira kucita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.
33 Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti cikukomereni, ndi kuti masiku anu acuruke m'dziko limene mudzakhala nalo lanu lanu.