4 Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,
5 (ndinalinkufma pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munacita mantha cifukwa ca moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:
6 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakuturutsa m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo.
7 Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.
8 Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;
9 usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate wao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
10 ndi kucitira cifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.