1 Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwacita m'dziko limene muolokerako kulilandira;
2 kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ace onse ndi malamulo ace, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu acuruke.
3 Potero imvani, Israyeli, musamalire kuwacita, kuti cikukomereni ndi kuti mucuruke cicurukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
4 Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;
5 ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.
6 Ndipo mau awa ndikuuzanilero, azikhala pamtima panu;