12 Ndipo kudzakhala, cifukwa ca kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwacita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani cipangano ndi cifundo cimene analumbirira makolo anu;
13 ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukucurukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi ana a nkhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.
14 Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu.
15 Ndipo Yehova adzakucotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa ziri zonse za Aigupto muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu.
16 Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawacitire cifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakucitirani msampha.
17 Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andicurukira; ndikhoza bwanji kuwapitikitsa?
18 musamawaopa; mukumbukile bwino cimene Yehova Mulungu wanu anacitira Farao, ndi Aigupto wonse;