3 Ndipo musakwatitsane nao; musampatsemwana wace wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wace wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.
4 Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu yina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.
5 Koma muzicita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.
6 Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.
7 Yehova sanakondwera nanu, ndi kukusankhani cifukwa ca kucuruka kwanu koposa mitundu yonse yina ya anthu, kapena kucepera kwanu;
8 koma Yehova anakuturutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, cifukwa Yehova akukondani, ndi cifukwa ca kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.
9 Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.