15 Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nazo pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza.
16 Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yaucimo, ndipo, taonani, adaitentha.
17 Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati, Mwalekeranji kudya nsembe yaucimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulikitsa, ndipo iye anakupatsani iyo, kucotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwacitira cowatetezera pamaso pa Yehova?
18 Taonani, sanalowa nao mwazi wace m'malo opatulika m'katimo; mukadaidyera ndithu m'malo opatulika, monga ndinakuuzani.
19 Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yaucimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yaucimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova?
20 Pamene Mose adamva ici cidamkomera pamaso pace.