4 Ndipo Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwacotse pakhomo pa malo opatulika kumka nao kunja kwa cigono.
5 Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawabvula maraya ao a m'kati, kumka nao kunja kwa cigono, monga Mose adauza.
6 Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi ltamara ana ace, Musawinda tsitsi, musang'amba zobvala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israyeli, alire cifukwa ca motowu Yehova anauyatsa.
7 Ndipo musaturuka pakhomo pa cihema cokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anacita monga mwa mau a Mose.
8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,
9 Usamamwa vinyo, kapena coledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'cihema cokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;
10 ndi kuti musiyanitse pakati pa copatulika ndi cosapatulika, ndi pakati pa codetsa ndi coyera;