26 Nyama iri yonse yakugawanika ciboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; ali yense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
27 Ndipo iri yonse iyenda yopanda ciboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; ali yense wokhudza mtembo wace adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
28 Ndipo iye amene akanyamula mtembo wace atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.
29 Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wace;
30 ndi gondwa, ndi mng'anzi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi mfuko.
31 Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; ali yense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
32 Ndipo ciri conse cakufa ca izi cikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale cipangizo camtengo, kapena cobvala, kapena cikopa kapena thumba, cipangizo ciri conse cimene agwira naco nchito, acibviike m'madzi, ndipo cidzakhala codetsedwa kufikira madzulo; pamenepo cidzakhala coyera.