27 ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lace lamanzere ndi cala cace ca dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;
28 ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lace pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa cala cacikuru ca: dzanja lace lamanja, ndi pa cala cacikuru ca phazi lace la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa usembe yoparamula;
29 ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumcitira comtetezera pamaso pa Yehova.
30 Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yaucimo, ndi tina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa;
31 ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova.
32 Ici ndi cilamulo ca iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pace.
33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,