29 ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumcitira comtetezera pamaso pa Yehova.
30 Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yaucimo, ndi tina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa;
31 ndipo wansembe amcitire comtetezera pamaso pa Yehova.
32 Ici ndi cilamulo ca iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pace.
33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
34 Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanu lanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanu lanu;
35 pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.