1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;
2 ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsaru yocinga, pali cotetezerapo cokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pacotetezerapo.
3 Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.
4 Abvale maraya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zobvala za kumiyendo pathupi pace, nadzimangire m'cuuno ndi mpango wabafuta, nabvale nduwira yabafuta; izi ndi zobvala zopatulika; potero asambe thupi lace ndi madzi, ndi kubvala izi.
5 Ndipo ku khama la ana a Israyeli atenge atonde awiri akhale a nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.