1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Ine ndine Yehova Molungu wanu.
3 Musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Aigupto muja munakhalamo; musamacita monga mwa macitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.
4 Muzicita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.