15 Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israyeli, zopereka iwo kwa Yehova;
16 ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwaparamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
18 Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana onse a Israyeli, nuti nao, Ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena wa alendo ali m'Israyeli, akabwera naco copereka cace, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
19 kuti mulandiridwe, azibwera navo yaimuna yopanda cirema, ya ng'ombe, kapena nkhosa, kapena mbuzi.
20 Musamabwera nayo yokhala ndi cirema; popeza siidzalandirikira inu.
21 Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa cowinda cacikuru, kapena ya pa copereka caufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda cirema.