24 Nyama yofula, kapena copwanya kapena cosansantha, kapena cotudzula, kapena codula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamacicita ici m'dziko mwanu.
25 Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale cakudya ca Mulungu wanu; popeza ziri nako kubvunda kwao; ziri ndi cirema; sizidzalandirikira inu.
26 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi mace masiku asanu ndi awiri;
27 kuyambira tsiku lacisanu ndi citatu ndi m'tsogolo mwace, idzalandirika ngati copereka nsembe yamoto ya Yehova.
28 Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wace tsiku limodzimodzi.
29 Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.
30 Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.