6 munthu wokhudza ciri conse cotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lace ndi madzi.
7 Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pace adyeko zoyerazo, popeza ndizo cakudya cace.
8 Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.
9 Potero asunge cilangizo canga, angasenzepo ucimo, ndi kufera m'mwemo, pakuciipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo,
10 Mlendo asadyeko copatulikaco; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa nchito, asadyeko copatulikaco.
11 Koma wansembe atakagula munthu ndi ndarama zace, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yace, adyeko mkate wace.
12 Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.