19 Munthu akacititsa mnansi wace cirema, monga umo anacitira momwemo amcitire iye;
20 kutyola kulipa kutyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anacitira munthu cirema, momwemo amcitire iye.
21 Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere yina; iye wakupha munthu, amuphe.
22 Ciweruzo canu cifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
23 Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo anaturutsa wotembererayo kunja kwa cigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yehova adauza Mose.