35 Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi dzanja lace lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.
36 Usamambwezetsa phindu, kapena cioniezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.
37 Musamampatsa ndarama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pocibwezera.
38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.
39 Ndipo mbale wako akasaukira cuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa nchito monga kapolo;
40 azikhala nawe ngati wolipidwa nchito, ngati munthu wokhala nawe; akutumikire kufikira caka coliza lipenga.
41 Pamenepo azituruka kukucokera, iye ndi ana ace omwe, nabwerere ku mbumba yace; abwerere ku dziko lao lao la makolo ace.