40 azikhala nawe ngati wolipidwa nchito, ngati munthu wokhala nawe; akutumikire kufikira caka coliza lipenga.
41 Pamenepo azituruka kukucokera, iye ndi ana ace omwe, nabwerere ku mbumba yace; abwerere ku dziko lao lao la makolo ace.
42 Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.
43 Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.
44 Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo amuna ndi akazi.
45 Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anu anu.
46 Ndipo muwayese colowa ca ana anu akudza m'mbuyo, akhale ao ao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israyeli, musamalamulirana mozunza.