1 Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena coimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
2 Musunge masabata anga, ndi kucitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.
3 Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita;
4 ndidzakupatsani mvula m'nyengo zace, ndi dziko lidzapereka zipatso zace, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zace.