1 Ndipo akacimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osaulula, azisenza mphulupulu yace;
2 kapena munthu akakhudza ciri conse codetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa coweta codetsa, kapena mtembo wa cokwawa codetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi woparamula.
3 Kapena akakhudza codetsa ca munthu, ndico codetsa ciri conse akakhala codetsedwa naco, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula:
4 kapena munthu akalumbira ndi milomo yace osalingirira kucita coipa, kapena kucita cabwino, ciri conse munthu akalumbira osalingirira, ndipo cidambisikira; koma pocizindikira akhala woparamula cimodzi ca izi: