2 Akacimwa munthu nakacita mosakhulupirika pa Yehova nakacita monyenga ndi mnansi wace kunenaza coikiza, kapena cikole, kapena cifwamba, kapena anasautsa mnansi wace;
3 kapena anapeza cinthu cotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa cimodzi ca izi zonse amacita munthu, ndi kucimwapo;
4 pamenepo padzali kuti popeza anacimwa, naparamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwacifwamba, kapena cinthuci adaciona ndi kusautsa mnzace, kapena coikiza anamuikiza, kapena cinthu cotayika anacipeza;
5 kapena ciri conse analumbirapo monama; acibwezere conseci, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ici kwa mwini wace tsiku lotsutsidwa iye.
6 Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola mwace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula, adze nayo kwa wansembe;
7 ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena ziti zonse akazicita ndi kuparamula nazo.
8 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,